Psalms 40

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Mofatsa ndinadikira Yehova
Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
2Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,
mʼthope ndi mʼchithaphwi;
Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe
ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
3Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,
nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.
Ambiri adzaona,
nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.

4Ndi wodala munthu
amakhulupirira Yehova;
amene sayembekezera kwa odzikuza,
kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
5Zambiri, Yehova Mulungu wanga,
ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.
Zinthu zimene munazikonzera ife
palibe amene angathe kukuwerengerani.
Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,
zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

6Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,
koma makutu anga mwawatsekula;
zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo
Inu simunazipemphe.
7Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.
Mʼbuku mwalembedwa za ine.
8Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;
lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”

9Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;
sinditseka milomo yanga
monga mukudziwa Inu Yehova.
10Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;
ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.
Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu
pa msonkhano waukulu.

11Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.
12Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira;
machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona.
Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga,
ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.

13Pulumutseni Yehova;
Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.
14Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga
achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene amakhumba chiwonongeko changa
abwezedwe mwamanyazi.
15Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!”
abwerere akuchita manyazi.
16Koma iwo amene amafunafuna Inu
akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”

17Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa;
Ambuye andiganizire.
Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga;
Inu Mulungu wanga, musachedwe.
Copyright information for NyaCCL